Members Login
Username 
 
Password 
    Remember Me  
Post Info TOPIC: NDAKATULO


Newbie

Status: Offline
Posts: 44
Date:
NDAKATULO
Permalink Closed


Kumbukirani abwenzi mwataya
Omwe mudakonda kuseleulana nao pa lamya
Lero, kulibe onsewa
Mathumba kuli chete adawameza.
ndiye mukamagwirana pa phewa
Ndi amuna aweni
Pena akazi aweni
Mudzikumbuka kuti nthawi yochita masewero
Siyino ayi
Mtheradi ndimvereni abale anzanga
mukamadya zakudya zabwino
Vinyo wodula ati Khristala ali thoo mudzikho
Nyama yootcha ikutokosa nkhwiru
Kumbukirani achibale kuti
Adaliko a mnzanu a mau akucha
Anamwali odziwa kusamba adalidzaza dzikoli
lero mbambadi kulibe onsewa
Yambani mwaima kaye
Mulingalire mozama
Apo ayi
Idzakakwanira EDZI muthupi lako
Udzaperepeseka iwe
Ngati chikolopa
Udzachakachika umo lithera curtain la bachelor ku Ndirande.
Ali ndi mwana agwiritse
Poti ngati simumva anthuni
Mudzalilira ku utsi
Mukunong'oneza bondo
Kumati
Ondiuza ndiye analipo
Kumbukirani mau awatu
Wakutsina khutu ndi mnansi
Pajatu sikadza kokha
kaopa kulaula.

(Adapted from the works of Okoma atani Malunga)

__________________
Page 1 of 1  sorted by
 
Quick Reply

Please log in to post quick replies.

Tweet this page Post to Digg Post to Del.icio.us


Create your own FREE Forum
Report Abuse
Powered by ActiveBoard